Masipeya ndi Kakonzedwe

Zinthu zonse a SMAG apanga ndikugwiritsidwa zimakhala ndi mwayi okonzedwa kapena kupereka uphungu kumadera onse kumene muliko. Ife timayesetsa kuti muthandizike mwansanga msanga masandi usiku.

A SMAG anakwaniritsa kulandila masatifiketi osiyana siya chifukwa chaukadaulo wawo popanga zinthu zabwino, kusamalira ogwira ntchito awo komanso kuthandiza anthu amene akugwiritsa zinthu zawo. Masatifiketi monga awa anaperekedwa : ku ISO 9001 ya Quality Management; ISO 14001 ya Environmental Management System, OHSAS 18001 potsatira Occupational health & safety, ISO10002 pa nkhani yodziwa kusamarila makasitomala ndiponso ISO 27001pa Information Security. Ma tsamba onsewa anaperekedwa kwa AlGhandi ataunikidwa kuti iwo amasata bwino nkhani zosamalira chilengedwe, kusamalira makasitomala awo powapangira zinthu zolimba ndiponso zowoneka bwino. Iwonso amatamandika chifukwa chakuyang’anira bwino ogwira ntchito awo powapasa malo abwino ogwirira ntchito.

Kuli konse komwe a SMAG akupezeka amakhala ndi wekishopu yokhala ndi zinthu izi:

-Athu ophunzira bwino pankhani yokonza zinthu zomwe amapanga a SMAG

-Zida zawo zogwiritsa ntchito zimakhala zamakono zomwe zimakonzedwa pafupi pafupi

-Makina apamwamba owunikira vuto la chinthu chomwe chavuta

-Amakhala ndi ma sipeya pati osiyana siyana kuti inu muthandikizike

-Anthu ogwira ntchito masana ndi usiku

-Amatha kumasula injini yonse ndi kuyikonzanso mwasopano

-Amakhala ndi anthu amene amabwera kumene vuto lakupezerani

-ISO Certified Systems imayikidwa kutsimikiza kulimba kwa ntchito zawo

 

Palitu chifukwa cheni cheni chomwe mpofunika kuyikira masipeya eni eni osati a feki pamene mukhonzetsa galimoto yanu kwa magalaja athu. Ma sipaya patsi opangi ndi a SMAG amakhala olimba ndiposo opangidwa mwaukadaulo ndiponso a SMAG amakuthandizani ngati mungapeze mavuto ena ali onse.

Kodi mukuvutika kupeza ma sipeya patsi mukawafuna msanga msanga? Ifetu a SMAG vuto ili tinaliona kale ndipo yankho tinalipeza kale. Ife timapezeka ndi ma sipeya patsi amitundu wonse kuti inu musavutike pa nthawi yo mukuwafuna. Pajatu ife tima thandizanso masana ndi usiku inu mukakumana ndi vuto liri lonse.

Mau tingakuuzeni ndi akuti selevisi ndiyofunika kwa  chinthu chili chonse ngati tikufuna kuti moyo wa chinthucho utalike. Popanda selevisi katundu wanu sachedwa kutopa ndipo amayamba kugonja. Ichi chimakhala chiopyezo chifuka katunduyu amayamba kukudyerani ndalama zanu chifukwa kuonongeka kumabwera pafupi pafupi.

Mukakhala kuti mumagwiritsa akadaulo eni eni kokonza katundu wanu ndiponso muma gula ma sipeya patsi eni eni zimapangitsa kuti inu muzikhala ndi ufulu wamu mtima chifukwa simukayikira kapena kundera nkhawa  chifukwa mumadziwa kuti a SMAG akutsamalirani katundu wanu.