CRAWLER EXCAVATOR

Fomu yofunsira

Makinawa adapangidwanso kachiwiri pofuna kuti akhale okhalitsa ndi odalirika ngakhale atagwiritsidwa ntchito yochuluka.

KUKHALITSA

Monga takamba kale, makinawa adakonzedwanso pofuna kuti afanane ndi kagwiridwe ntchito ka hydraulic pofuna kuti akhale wokhalitsa ndi wodalirika mu nyengo zones. Hydraulic Filter wanyuwani  amachepetsa kuwonongeka,kuchepetsa ndalama zowonong pokonzetsera makina komanso kuthandia kuti makinawa akhalitse.

KUSABOOLA MNTUMBA POKONZETSA

Makinawa adapangidwa moti asamatenge nthawi komanso ndalama zambiri pokonzetsa akawonongeka

MPHAMVU KOMANSO CHANGU

Monga takambira, makinawa ali ndi hydraulic system yomwe in ndi njira zitatu zogwilira ntchito zomwe zimathandiza kuti adzigwira ntchito mwachangu mokwera ndi 5 percent pakagwiridwe kake ka ntchito. Kamba koti makinawa ali ndi njira yowonera mulingo wa kathamangidwe komanso mphamvu zomwe amagwilira ntchito, mafuta amawonongeka ochepa poyerekeza ndi makina ena zomwe zimakomera anthu omwe akuwagwiritsa ntchito.

KUGWIRITSIDWE NTCHITO KOSAVUTA

Mmene makinawa adakonzedwera amapereka mpata wabwino woti miyendo komanso mapazi atha kugwira ntchito motakasuka.Makinawa amakhalanso ndi timadzi tomwe timathandiza kuti makinawa aziyenda mosavuta zomwe zimachititsa kuti owagwiritsa ntchito asamatope mwachangu

CHITETEZO KWA OWAGWIRITSA NTCHITO

Kupatula kuti makinawa anapangidwa moti asamachite pohokoso komanso kunjenjemera kwambiri, Ogwiritsa ntchito makinawa ali ndi ufulu woyika mulingo wa momwe akufunira kuti makinawa adzigwilira ntchito zomwe ndizothandiza kuti moyo wa munthuwo usakhale pa chiopsezo chifukwa amakhala kuti akudziwa mmene makina ake akuyendera.

المواصفات :

  • Kapangidwe : CX210B LC
  • Engine : Isuzu - Tier 3
  • Mphamvu : 117 kW / 157 hp
  • Kulemera (kg) : 21.3 t